THE REVIEW OF THE WORLD'S BIGGEST BANK ROBBERY (Chichewa Vision)


.*THE GOLD DIGGERS*
.
_Banco Central burglary at Fortaleza_
.
*operation banco*.
.
KODI MBAMVA ZODABWITSA ZITABA NDALAMA ZODZADZA 3 TANI(3 TONS) MU BANK INA KU BRAZIL MU CHAKA CHA 2005 ZIDATHA BWANJI?
.
Mu chaka cha 2005 Ku mzinda wa *Fortaleza* mu dziko la Brazil kudachitikapo umbava waukulu umene udadzidzimutsa anthu pano pa dziko lapansi lonse, ku mzinda umenewu mbanva zidalowa bank ina mwaukadaulo zedi mkubamo ndalama zankhaninkhani mpaka zodzadza galimoto ija ya 3 ton.
.
Ena akuti iwe mzungu wakuda, wangoyiyamba nkhaniyi ifetu mzinda wa Fortaleza sitikuudziwa, uli kutikuti???
Mzungu Wakuda pa Star Walero Family, inuyo tangodekhani phuma ayi
.
*Fortaleza*
.
uwu ndi mzinda waukulu kwambiri kapena kuti capital city ya state kapena kuti dera lotchedwa Ceará mu dziko la Brazil, ku mpoto kwa mzindau kuli Atlantic Ocean, kummwera kwake kuli ma municipality a *Pacatuba* ,
*Eusébio*, *Maracanaú* ndi *Itaitinga* pomwe ku mmawa kwake kuli municipality yotchedwa *Aquiraz*. mzindau uli ndi ma factory komanso ndi umodzi mwa mizinda ikuluikulu yomwe kumapangika ma business akuluakulu mu dziko la Brazil, mzindau unakhazikitsidwa Pa April 13, mu chaka cha 1726, city yi ndi imodzi mwa ma city akuluakulu komanso olemera kwambiri pa dziko lapansi pano ndipo mu 2014 Fifa World Cup idaseweredwa mu mzindawu.
Pokhala city yapamwamba kwambiri, mu mzindau munakhazikitsidwa nthambi zingapo za ma bank osiyanasiyana, ndipo nthambi ya bank ina yaikulu kwambiri yomwe imatchedwa *Banco Central* inakhazikitsidwanso mu mzindawu.
.
Mu chaka cha 2005, (Mzungu Wakuda akuyera) mbava zomwe anthu amaziganizira kuti ndi ma engineer akuluakulu, zidakalowa ndi kuba mu bank yi, koma mabedwe ake adadzidzimutsa dziko lonse lapansi chifukwa cha plan yodabwitsa yomwe mbavazo zidapanga.
Kodi mbavazi zidaba bwanji kuti robbery(,umbava) yawo iikidwe pa *world greatest bank robbery*???
Inu musachoke Mzungu Wakuda wayamba kuyera tsopano.
.
Pa 8 August, tsikuli lomwe lidali lolemba, Monday, mu chaka cha 2005, ogwira ntchito mu *Banco central* mmamawa atatsekula bank yawo adadzidzimuka kupezamo chidzenje chachikulu, ataonetsetsa bwinobwino adaona kuti ndalama zonse mulibe mu bank, inde ndalama zankhaninkhani zabedwa.


Part 2 Is Coming Soon

Comments

Popular posts from this blog

Airtel money reduces cash out fees to Malawi customers