Chilima Wapereka Mpata Wa Matsiku 30 Kuti Bungwe Logawa Madzi Kuchigawo Cha Ku M'mwela Lithane Ndi Vuto Lakusowa Kwa Madzi

Image may contain: outdoor

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Saulosi Chilima wapereka mpaka pa 2 October kuti bungwe logawa madzi kuchigawo cha ku m'mwela lithane ndi vuto lakusowa kwa madzi.

Chilima yemwe ndi nduna yowona za kusintha kwa kagwilidwe ntchito ka m'boma wanena izi atakumana ndi akuluakulu a bungweli.

Chilima wati ndi sozamveka kuti anthu azikhala opanda madzi kwa masiku oposa awiri mpaka tsabata opanda madzi.

Iye wati akuyenbekeza kuti kusowa kwa madzi kukhala mbiri yakale pomafika pa 2 October chaka chino pomwe bungwe logawa madzili lalonjeza kuthana ndi vutoli m'masiku makumi atatu.

Comments

Popular posts from this blog

Airtel money reduces cash out fees to Malawi customers