MTSIKANA WA ZAKA 18 AKAKHALA KU NDENDE KWA ZAKA ZIWIRI PA MLANDU WOKUBA MWANA WA NKHANDA
Bwalo la milandu la Phalombe First Grade Magistrate lalamula mtsikana wa zaka 18 kukakhala ku ndende kwa zaka ziwiri (2) pa mlandu wokuba mwana wa nkhanda yemwe anali atangobadwa kumene.
Mtsikanayo anaba mwanayo pa 29 August 2020 pa chipatala cha Holy Family Mission.
Mtsikanayo anaberekera mwana wake pa chipatalacho koma mwanayo anamwalira atangobadwa kumene zomwe zinapangitsa mtsikanayo kuba mwana wa nkhanda wa munthu wina.
Mtsikanayo dzina lake ndi Esther Brighton.
Comments
Post a Comment