BAMBO WA ZAKA 35 WAMANGIDWA ATAPEZEKA NDI NDALAMA ZA CHINYENGO
Apolisi dzulo m'boma la Kasungu amanga a Filodi Goodson Chifukwa chopezeka ndi ndalama za pepala zomwe ndima Mk 2,000 achinyengo zokwana Mk 320,000.
Munthuyo wamangidwa m'mudzi mwa Vijumo T/A Mwase m'bomalo.
Anthu ena anadziwitsa apolisi kuti Mkuluyo anagona pa malo ogonako alendo a Midima komanso anati Mkuluyo anali ndi ndalama za chinyengo zomwe zinachititsa apolisi kuchita kafukufuku mpakana apolisiwo anapita ku maloko komwe anazipeza ndalamazo kuchokera kwa Mkuluyo.
Ndalamazo zinali ndi nambala yofana ya AT4426785.
Goodson amachokera m'mudzi mwa Ngolovani T/A Nsakambewa m'boma la Dowa.
Comments
Post a Comment