MLONDA WINA AKAKHALA KU NDENDE KWA MIYEZI 30 CHIFUKWA ANATHYOLA MU OFESI YOMWE AMKAYANG'ANIRA
Bwalo la milandu la Nkhunga First Grade Magistrate lalamula kuti a MacDonald Mussa a zaka 28 akakhale ku ndende kwa miyezi yokwana 30 Chifukwa choti anathyola ofesi yomwe amkayang'anira ndikubamo kompyuta.
Bamboyo amagwira ntchito ngati mlonda wa chitetezo ku kampani yopereka chitetezo ya GardaWorld Security.
Pa usiku wapa 29-30 August 2020, bamboyo anapatsidwa ntchito yoyang'anira ma ofesi aku kampani ya Illovo ku Dwangwa.
Bamboyo anathyola ofesi imodzi momwe anatengamo kompyuta ya ndalama zokwana Mk 360,000.
Tsiku lotsatilalo ayini ake a ofesiyo anadabwa kuwona kuti kompyuta inali itasowa mpakana mlondayo anamangidwa komanso kompyutayo inapezeka ndi mlondayo.
Mlondayo anakawonekera ku bwalo la milandu pa 7 September 2020 komwe amulamula kukakhala ku ndende kwa miyezi yokwana 30.
MacDonald Mussa amachokera m'mudzi mwa Mavwere T/A Mavwere m'boma la Mchinji.
Comments
Post a Comment